Mtonga Isaac Pharmacy Online

-->
Skip to main contentMtonga Isaac Pharmacy is Health and Medical facility that manufacture Herbal medicines at Traditional level and provides treatment to so many kinds of diseases. This Health facility is based on Herbal medicines rather than Drugs to maintain good health. It is branded by Dr. Mtonga N. Isaac (Herbalist) in Lusaka capital city of Zambia, African region. This business name was registered on 23rd March, 2022 according to Act No: 16 of 2011 of the Laws of Zambia.
Ndiwo mwambi wakuletsa zakunama ngati munthu wina aulula za mnzache kuleka zache. Tamvani nthanoyi:
Tsiku lina munthu anapita kuthengo kukafuna nyama, napha tiana tiwiri ta Kalulu. Pakubwera nthawi yamadzulo, anamva kumudzi kwao anthu analikuchita phokoso.
Pofika pafupi ndi mudzi anakomana ndi Mkango utasenza mwana wa mfumu (Village Headman).
*Iye anaopa koma mkango unafunsa nati, "Kodi uchokera kuti??
*Iye anati,"Ndichokera kuthengo."
*Mkango Unati, "Usamati, 'Ndichokera kuthengo', koma udziti, Ndichokera kwanu'."
*Munthu uja anabvomereza ndi mantha nati, "Pepani Bambo, ndichokera kwanu."
*Mkango unati, "Kodi ndiko watenga nyamazi?"
*Iye anati, "Inde."
*Mkango unati, "Inenso ndafumira kwanu ndiko ndatenga kamwana ka Headman aka."
Pompo unauza munthu uja kumuchenjeza kuti, "Tsono iwe, takomana alenje(olakwa) okha-okha ndipo ulenje usamasimba wa mnzako koma wako."
Tsono anasiyana, wina napita kwao winanso kwao.
Munthu uja atafika kwao anaika nyama zake m'nyumba yake, natulukira panja nafunsa anthu kuti,
*"Kodi mulirira chiani?"
*Iwo anati, "Mwana wa Bambo wagwidwa ndi Mkango."
*Iye anayamba kusimba ulenje wa mnzake nati, "Ine ndakomana nawo Mkangowo utatenga mwana wa mfumuyo."
*Koma nthawi imeneyo mkango uja unali pafupi ndi mudzi ndipo unamva mau ache.
*Mkango unaomba m'manja nugwira pakamwa nuti,
*"Kodi wolakwa ndine apa ndatenga kanyama kwake. Iye kwathu watengako nyama ziwiri, ha! chabwino."
Munthu uja anauza anthu kumene unalowera nautsata onse pamodzi. Koma Mkangowo unalowa m'nyumba yake ya munthu uja nugoneka mwana uja pamalo pamene anaika nyama zake nutenga nyamazo nusiyapo mwana wakufayo.
Koma anthu aja pobwera atalephera kumene anautsata mkangowo, anakumbukira msanga tinyama tija popeza inawagwira nkhuli, nati,
"Tiye ukatipatseko kanyama tikadyere ku maliro."
Popita anapeza mwana wa mfumuyo ali gone wakufa! Anthu aja anati,
"Kodi ndiye Kalulu uja wapha ku thengo?"
Iyenso anadabwa ndithu, koma anthu anamgwira namumenya kufikira atafa.
*Ndimo akhalira manena-nena: Ulenje umasimba wako, wamnzako ai.
Mwambi uwu umaponyedwa pa mirandu ngati munthu wina wochimwa amayamba kuulula uchimo wa mnzake, wake ndi kubisa, mnzake namayambanso kuulula uchimo wa iye.
Pompo ndi pamene panadzera mwambi umenewu poona kuti onse ali ochimwa (monga kuti onse ali osaka kapena alenje ndipo sikwabwino kunenetsa za ulenje wa mnzake. Simba zako osati za mzako ai.
KONKHANI MIYAMBI YINA PASIPA
____________________________________________________________
Contact us:
Mtonga Isaac Pharmacy,
Ng'ombe Township,
#16/24 Off Zambezi road,
Email: mtongaisaacpharmacy@gmail.com,
Tel: +260974272433/+260966399444,
Lusaka, Zambia .
_______________________________________ _______________________________________