Mtonga Isaac Pharmacy Online

-->
Skip to main contentMtonga Isaac Pharmacy is Health and Medical facility that manufacture Herbal medicines at Traditional level and provides treatment to so many kinds of diseases. This Health facility is based on Herbal medicines rather than Drugs to maintain good health. It is branded by Dr. Mtonga N. Isaac (Herbalist) in Lusaka capital city of Zambia, African region. This business name was registered on 23rd March, 2022 according to Act No: 16 of 2011 of the Laws of Zambia.
Wina akanena mau opotoza poyamba anthu amamva msanga, ndipo iye akati akometsenso, anzache amati,
"Ai, ife tamva mau oyamba aja." Nthano yache ya mwambi uwu ndi iyi:
*Nchenzi (Orter) ndi Mkango anapangana chibwenzi. Analikukhala m'malo osiyana wina kwina, wina kwina.
Chaka china nchenzi inatuma mthenga kwa mkango kukapempha malo kuti ikhale nawo.
Iyo inauza mthenga wache niti, "Ukanka ukamvetse mau oyamba bwenzi wangayo ati akalankhule, mau omwewo adzasonyeza ngati iye ali ndi chikondi."
Popita mthenga kwa mkango ndi kulongosola mau onsewo, mkangowo unati poyamba,
"Abwere bwenzi wanga wokoma nchipwidza" ( kutanthauza kuti, wokoma kumudya ndi matumbo omwe osafinya).
Unatinso mau ena,
"Iwe ukapita kwa bwenzi Nchenzi, ukamuuze kuti ndikondwera kwambiri kukhala naye, ndiribe kanthu kena ai. Nsenjere iripo yambiri iyi, azidzadya."
Mthenga popita kwa nchenzi sananene za mau oyamba aja ai, koma achiwiriwo.
Nchenzi pakumva inati, "Ine ndifunitsa kumva mau oyamba, asananene awa."
Mthenga uja analephera kukana anati,
"Koma mau wandiuza Mkango kuti ndidzanene ndi amenewa."
Nchenzi pofunsitsabe wamthengayo anati,
"Pali mau ena amene sanandiuze kudzanena amene ndinaganiza kuti amangonena yekha ndiwo anati,
"Abwere bwenzi wanga wokoma nchipwidza."
Nchenzi pomva mau awa anati, "Nanga tamvera iwe, ukudziwa mau amenewa kutanthauza kwache?
Iye afuna kuti ine ndikapita akandidye."
KONKHANI MIYAMBI YINA PASIPA
_____________________________________________________________
Contact us:
Mtonga Isaac Pharmacy,
Ng'ombe Township,
Email: mtongaisaacpharmacy@gmail.com,
Tel: +260974272433/+260966399444,
Lusaka, Zambia .
_______________________________________ _______________________________________