NYANJA PROVERBS RE-EDITED BY DR MTONGA N. ISAAC
Kale-kale mitundu yonse ya anthu inali ndi zochita ndi zonena-nena za mitundu mitundu. Anali ndi zina zokambirana akulu okha-okha, zinanso zokambira ana
ao. Anali ndi nthanthi ndi miyambi ya mitundu-mitundu imene inali ndi ziphunzitso zosiyana-siyana.
Miyambi yina inali yonena pa mirandu mophiphiritsa koma yokhala ndi zolozera zache, kotero anthu nadziwa ponena. Yina inali yakuphunzitsa za chikhalidwe cha
anthu, za umphala, za pabanja, za nthenda, za imfa ndi zina zotero.
Zophunzira zambiri zinakolekedwa ku miyambi. Ngakhale sanadziwe kulemba ndi kuwerenga koma anangozikumbukira ponena-nena malinga ndi kanthu kache koonekera. Masiku ano miyambiyo imamveka kamodzi-kamodzi ikunenedwa ndi anthu. Ana ambiri a lero saidziwa chifukwa sinalembedwe.
Makolo athu anangopitiriza mwakungokamba mwa
mibadwo-mibadwo kufikira tsopano. Chifukwa cha chimenechi zambiri zangoferamo zosakumbukiridwa
chifukwa cha kubvuta kuzikumbukira m'mutu mokha.
Tayesa kusonkhanitsa miyambi imene iri yofunika ndi anthu ambiri kotero kuti ana a ana athu asadzaiwale nzeru zochitidwa kale ndi makolo ao koma apezemo maziko a nzeru zatsopano ndi zamtsogolo. Popanda
kudziwa miyambi yakale, tidzakhala anthu obvutika pophunzira zatsopano chifukwa chosowa popondera (maziko) polimba pamene makolo athu anatikonzera.
Miyambi yina yolembedwayi ingakhale yothangata oweruza a lero m'dziko lino pozenga mirandu yao, yina.
SANKHANI MWAMBI MUSIMU:
______________________________________________________________
Contact us:
Mtonga Isaac Pharmacy,
Ng'ombe Township,
#16/24 Off Zambezi road,
Email: mtongaisaacpharmacy@gmail.com,
Tel: +260974272433/+260966399444,
Lusaka, Zambia.
_______________________________________
_______________________________________
________________________________________
_______________________________________