BVUNDULA MADZI
Panali midzi iwiri yoyandikana. Midzi yonseyo inali kumwera pa chitsime chimodzi, ndipo anthu am'midzi yonseyo anali okondana.
Pafupi ndi chitsimecho panali
mtengo waukulu m'mene munali kukhala mbalame yosa dziwika dzina lake. Iyo inaganizira nzeru yochita kufuna kudanitsa anthu aja. Iyo inadza nibvundula madziwo ndi kuwadetsa(kufipitsa) kwambiri.
Pofika anthu a mudzi winawo anapeza matope okha-okha nadabwa kwambiri, koma anadziwa anzao aja anali pompo kudzatunga madzi, nayesa kuti ndi amene anadetsa.
Tsiku lina iwo anayamba kudzatunga madzi, mbalameyo niipenya. Atatha kuchoka iyo inabwera ndi kubvundula msanga-msanga nichokapo.
Pobwera ena aja anadabwa nawonso naganizira kuti ndi anzao anachita choncho. Zonenedwa pa mirandu
chimenecho.
Izi zinangochitikabe kufikira anthuwo
anangodana pachabe, ndipo pomalizira anasonkhana nanena mirandu. Iwo onse analikungokanirana.
Ndipo popeza anafuna kukhala okondana anati, "Tiyeni
tipezetu amene abvundula madzi timgwire."
Napangana kukhalira tsiku lina. Tsiku limenelo akazi atatha kutunga madzi ndi kuchoka, mbalameyo inadza nibvundula madziwo, amuna aja alikuyang'ana, nathamanga nthawi yomweyo naigwira nati,
"Kodi ndiwe ubvundula
madziwa?"
Iwo anaitenga naitanizana onse kuti adzaone Bvundula madzi, potsirizira naipha.
*Mwambi uwu umaponyedwa pa mirandu pamene anthu awiri adana, chotero amati,
"Tiyeni tiyambe tifune 'Bvundula madzi'."
KONKHANI MIYAMBI YINA MUSIMU:
______________________________________________________
Contact us:
Mtonga Isaac Pharmacy,
Ng'ombe Township,
#16/24 Off Zambezi road,
Email: mtongaisaacpharmacy@gmail.com,
Tel: +260974272433/+260966399444,
Lusaka, Zambia.
_______________________________________
_______________________________________
________________________________________
_______________________________________